1. Yehova, imvani cilungamo, mverani mpfuu wanga;Cherani khutu ku pemphero langa losaturuka m'milomo ya cinyengo,
2. Pankhope panu paturuke ciweruzo canga;Maso anu apenyerere zolunjika,
3. Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;Mwandisuntha, simupeza kanthu;Ndatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
4. Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanuNdingalowe njira za woononga.
5. M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu,Mapazi anga sanaterereka.
6. Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu:Cherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
7. Onetsani cifundo canu codabwiza, Inu wakupulumutsa okhulupirira InuKwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.