4. Zidzacuruka zisoni zao za iwo otsata mulungu wina:Sindidzathira nsembe zao zamwazi,Ndipo sindidzachula maina ao pakamwa panga,
5. Yehova ndiye gawo la colowa canga ndi cikho canga:Ndinu wondigwirira colandira canga,
6. Zingwe zandigwera mondikondweretsa;Inde cosiyira cokoma ndiri naco.
7. Ndidzadalitsa Yehova, amene anandicitira uphungu:Usikunso imso zanga zindilangiza.
8. Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse:Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
9. Cifukwa cace wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga;Mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
10. Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;Simudzalola wokondedwa wanu abvunde.
11. Mudzandidziwitsa njira ya moyo:Pankhope panu pali cimwemwe cokwanira;M'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.