Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 16:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.

2. Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga:Ndiribe cabwino cina coposa Inu.

3. Za oyera mtima okhala pa dziko lapansi,Iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli cikondwero canga conse.

4. Zidzacuruka zisoni zao za iwo otsata mulungu wina:Sindidzathira nsembe zao zamwazi,Ndipo sindidzachula maina ao pakamwa panga,

5. Yehova ndiye gawo la colowa canga ndi cikho canga:Ndinu wondigwirira colandira canga,

6. Zingwe zandigwera mondikondweretsa;Inde cosiyira cokoma ndiri naco.

7. Ndidzadalitsa Yehova, amene anandicitira uphungu:Usikunso imso zanga zindilangiza.

8. Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse:Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

9. Cifukwa cace wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga;Mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.

10. Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;Simudzalola wokondedwa wanu abvunde.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 16