Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 15:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, ndani adzagonera m'cihema mwanu?Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?

2. Iye wakuyendayo mokwanira, nacita cilungamo,Nanena zoonadi mumtima mwace.

3. Amene sasinjirira ndi lilime lace,Sacitira mnzace coipa,Ndipo satola msece pa mnansi wace.

4. M'maso mwace munthu woonongeka anyozeka;Koma awacitira ulemu akuopa Yehova.Atalumbira kwa tsoka lace, sasintha ai.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 15