Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 149:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Haleluya,Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano,Ndi cilemekezo cace mu msonkhano wa okondedwa ace.

2. Akondwere Israyeli mwa Iye amene anamlenga;Ana a Ziyoni asekere mwa Mfumu yao.

3. Alemekeze dzina lace ndi kuthira mang'ombe;Amyimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

4. Popeza Yehova akondwera nao anthu ace;Adzakometsa ofatsa ndi cipulumutso,

5. Okondedwa ace atumphe mokondwera m'ulemu:Apfuule mokondwera pamakama pao,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 149