Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 148:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mlemekezeni, m'mwambamwamba,Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.

5. Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.

6. Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;Anazipatsa cilamulo cosatumphika.

7. Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;

8. Moto ndi matalala, cipale cofewa ndi nkhungu;Mphepo ya namondwe, yakucita mau ace;

9. Mapiri ndi zitunda zonse;Mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:

10. Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse;Zokwawa, ndi mbalame zakuuluka;

11. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;Zinduna ndi oweruza onse a padziko;

12. Anyamata ndiponso anamwali;Okalamba pamodzi ndi ana:

13. Alemekeze dzina la Yehova;Pakuti dzina lace lokha ndi lokwezeka;Ulemerero wace uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.

14. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ace,Cilemekezo ca okondedwa ace onse;Ndiwo ana a Israyeli, anthu a pafupi pa Iye,Haleluya,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 148