Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 144:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime;Ana athu akazi ngati nsanamira za kungondya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

13. Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundu mitundu;Ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwi zikwi, inde zikwi khumi kubusako.

14. Kuti ng'ombe zathu zikhale zasenza katundu;Ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kuturukamo,Pasakhalenso kupfuula m'makwalala athu.

15. Odala anthu akuona zotere; Odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 144