Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 144:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,Wakuphunzitsa manja anga acite nkhondo,Zala zanga zigwirane nao:

2. Ndiye cifundo canga, ndi linga langa,Msanje wanga, ndi mpulumutsi wanga;Cikopa canga, ndi Iye amene ndimtama;Amene andigonjetsera anthu anga.

3. Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?Mwana wa munthu kuti mumsamalira?

4. Munthu akunga mpweya;Masiku ace akunga mthunzi wopitirira.

5. Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:Khudzani mapiri ndipo adzafuka.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 144