1. Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,Wakuphunzitsa manja anga acite nkhondo,Zala zanga zigwirane nao:
2. Ndiye cifundo canga, ndi linga langa,Msanje wanga, ndi mpulumutsi wanga;Cikopa canga, ndi Iye amene ndimtama;Amene andigonjetsera anthu anga.
3. Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?Mwana wa munthu kuti mumsamalira?
4. Munthu akunga mpweya;Masiku ace akunga mthunzi wopitirira.
5. Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:Khudzani mapiri ndipo adzafuka.
6. Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa;Tumizani mibvi yanu, ndi kuwapitikitsa,
7. Turutsani manja anu kucokera m'mwamba;Ndikwatuleni ndi kundilanditsa ku madzi akuru,Ku dzanja la alendo;
8. Amene pakamwa pao alankhula zacabe,Ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lacinyengo.
9. Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;Pa cisakasa ca zingwe khumi ndidzayimbira zakukulemekezani.
10. Ndiye amene apatsa mafumu cipulumutso:Amene alanditsa Davide mtumiki wace ku lupanga loipa.