5. Ndikumbukila masiku a kale lomwe;Zija mudazicita ndilingirirapo;Ndikamba pa ndekha za nchito ya manja anu.
6. Nditambalitsira manja anga kwa Inu:Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.
7. Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.Musandibisire nkhope yanu;Ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
8. Mundimvetse cifundo canu mamawa;Popeza ndikhulupirira Inu:Mundidziwitse njira ndiyendemo;Popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
9. Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;Ndibisala mwa Inu.
10. Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kucidikha.
11. Mundipatse moyo, Yehova, cifukwa ca dzina lanu;Mwa cilungamo canu muturutse moyo wanga m'nsautso.
12. Ndipo mwa cifundo canu mundidulire adani anga,Ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;Pakuti ine ndine mtumiki wanu.