Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 143:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Imvani pemphero langa, Yehova; ndicherere khutu kupemba kwanga;Ndiyankheni mwa cikhulupiriko canu, mwa cilungamo canu.

2. Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;Pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.

3. Pakuti mdani alondola moyo wanga;Apondereza pansr moyo wanga;Andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.

4. Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;Mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga,

5. Ndikumbukila masiku a kale lomwe;Zija mudazicita ndilingirirapo;Ndikamba pa ndekha za nchito ya manja anu.

6. Nditambalitsira manja anga kwa Inu:Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 143