Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 142:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Penyani ku dzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;Pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.

5. Ndinapfuulira kwa inu, Yehova;Ndina, Inu ndinu pothawirapo panga,Gawo langa m'dziko la amoyo.

6. Tamverani kupfuula kwanga; papeza ndisauka kwambiri;Ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.

7. Turutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;Olungama adzandizinga;Pakuti mudzandicitira zokoma.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 142