Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 140:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;

2. Amene adzipanga zoipa mumtima mwao;Masiku onse amemeza nkhondo.

3. Anola lilime lao ngati njoka;Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

4. Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.

5. Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe;Anacha ukonde m'mphepete mwa njira;Anandichera makwekwe.

6. Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.

7. Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga,Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.

8. Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.

9. Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,Coipa ca milomo yao ciwaphimbe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 140