Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 139:21-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova?Ndipo kodi sindimva nao cisoni iwo akuukira Inu?

22. Ndidana nao ndi udani weni weni:Ndiwayesa adani.

23. Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;Mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.

24. Ndipo mupenye ngati ndiri nao mayendedwe oipa,Nimunditsogolere pa njira yosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 139