Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 139:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.

2. Inumudziwakukhalakwangandi kuuka kwanga,Muzindikira lingaliro langa muli kutali.

3. Muyesa popita ine ndi pogona ine,Ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.

4. Pakuti asanafike mau pa lilime langa,Taonani, Yehova, muwadziwa onse.

5. Munandizinga kumbuyo ndi kumaso,Nimunaika dzanja lanu pa ine.

6. Kudziwa ici kundilaka ndi kundidabwiza:Kundikhalira patali, sindifikirako.

7. Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 139