Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 137:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pa msondodzi uli m'mwemo Tinapacika mazeze athu.

3. Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo,Ndipo akutizunza anafuna tisekere,Ndi kuti, Mutiyimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.

4. Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya YehovaM'dziko lacilendo?

5. Ndikakuiwalani, Yerusalemu,Dzanja lamanja langa liiwale luso lace.

6. Lilime langa limamatike ku nsaya zanga,Ndikapanda kukumbukila inu;Ndikapanda kusankha YerusalemuKoposa cimwemwe canga copambana.

7. Yehova, kumbukilani ana a EdomuTsiku la Yerusalemu;Amene adati, Gamulani, gamulani,Kufikira maziko ace.

8. Mwana wamkazi wa ku Babulo, iwe amene udzapasulidwa;Wodala iye amene adzakubwezera cilangoMonga umo unaticitira ife.

9. Wodala iye amene adzagwira makanda ako,Ndi kuwaphwanya pathanthwe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 137