Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 137:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ku mitsinje ya ku Babulo,Kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira,Pokumbukila Ziyoni.

2. Pa msondodzi uli m'mwemo Tinapacika mazeze athu.

3. Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo,Ndipo akutizunza anafuna tisekere,Ndi kuti, Mutiyimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.

4. Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya YehovaM'dziko lacilendo?

5. Ndikakuiwalani, Yerusalemu,Dzanja lamanja langa liiwale luso lace.

6. Lilime langa limamatike ku nsaya zanga,Ndikapanda kukumbukila inu;Ndikapanda kusankha YerusalemuKoposa cimwemwe canga copambana.

7. Yehova, kumbukilani ana a EdomuTsiku la Yerusalemu;Amene adati, Gamulani, gamulani,Kufikira maziko ace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 137