Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 136:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Naturutsa Israyeli pakati pao;Pakuti cifundo cace ncosatha.

12. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka:Pakuti cifundo cace ncosatha.

13. Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.

14. Napititsa Israyeli pakati pace;Pakuti cifundo cace ncosatha.

15. Nakhutula Farao ndi khamu lace m'Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.

16. Amene anatsogolera anthu ace m'cipululu:Pakuti cifundo cace ncosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 136