1. Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino:Pakuti cifundo cace ncosatha.
2. Yamikani Mulungu wa milungu:Pakuti cifundo cace ncosatha.
3. Yamikani Mbuye wa ambuye:Pakuti cifundo cace ncosatha.
4. Amene yekha acita zodabwiza zazikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
5. Amene analenga zakumwamba mwanzeru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
6. Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi:Pakuti cifundo cace ncosatha.
7. Amene analenga miuni yaikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
8. Dzuwa liweruze usana:Pakuti cifundo cace ncosatha.
9. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;Pakuti cifundo cace ncosatha.
10. Iye amene anapandira Aaigupto ana ao oyamba:Pakuti cifundo cace ncosatha.
11. Naturutsa Israyeli pakati pao;Pakuti cifundo cace ncosatha.
12. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka:Pakuti cifundo cace ncosatha.