Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 132:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,

9. Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.

10. Cifukwa ca Davide mtumiki wanuMusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

11. Yehova analumbira Davide zoona;Sadzalibweza; ndi kuti,Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wacifumu wako.

12. Ana ako akasunga cipangano cangaNdi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa,Ana aonso adzakhala pa mpando wanu ku nthawi zonse,

13. Pakuti Yehova anasankha Ziyoni;Analikhumba likhale pokhala pace; ndi kuti,

14. Pampumulo panga mpano posatha:Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.

15. Ndidzadalitsatu cakudya cace;Aumphawi ace ndidzawakhutitsa ndi mkate.

16. Ndipo ansembe ace ndidzawabveka ndi cipulumutso:Ndi okondedwa ace adzapfuulitsa mokondwera.

17. Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga;Ndak onzeraru wodzozedwa wanga nyali.

18. Ndidzawabvekaadani ace ndi manyaziKoma pa iyeyu korona wace adzambveka.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 132