5. Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?
6. Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.
7. Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.
8. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,
9. Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.
10. Cifukwa ca Davide mtumiki wanuMusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.
11. Yehova analumbira Davide zoona;Sadzalibweza; ndi kuti,Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wacifumu wako.
12. Ana ako akasunga cipangano cangaNdi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa,Ana aonso adzakhala pa mpando wanu ku nthawi zonse,