Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 131:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, mtima wanga sunadzikuzaNdi maso anga sanakwezeka;Ndipo sindinatsata zazikuru,Kapena zodabwiza zondiposa.

2. Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga;Ngati mwana womletsa kuyamwa amace,Moyo wanga ndiri nao ngati mwana womletsa kuyamwa.

3. Israyeli, uyembekezere Yehova,Kuyambira tsopano kufikira kosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 131