Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 13:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mudzandiiwala ciiwalire, Yehova, kufikira liti?Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?

2. Ndidzacita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti,Pokhala ndi cisoni m'mtima mwanga tsiku lonse?Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?

3. Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga:Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;

4. Kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka;Ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.

5. Koma ine ndakhulupira pa cifundo canu;Mtima wanga udzakondwera naco cipulumutso canu:

Werengani mutu wathunthu Masalmo 13