Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 129:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Yehova ndiye wolungama;Anadulatu zingwe za oipa.

5. Acite manyazi nabwerere m'mbuyo.Onse akudana naye Ziyoni.

6. Akhale ngati udzu womera patsindwi,Wakufota asanauzule;

7. Umene womweta sadzaza nao dzanja lace,Kapena womanga mitolo sakupatira manja.

8. Angakhale opitirirapo sanena,Dalitso la Mulungu likhale pa inu;Tikudalitsani m'dzina la Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 129