Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 126:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni,Tinakhala ngati anthu akulota.

2. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera;Pamenepo anati mwa amitundu,Yehova anawacitira iwo zazikuru,

3. Yehova anaticitira ife zazikuru;Potero tikhala okondwera.

4. Bwezani ukapolo wathu, Yehova,Ngati mitsinje ya ku Mwera.

5. Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.

6. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 126