Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 118:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Anene tsono nyumba ya Aroni,Kuti cifundo cace ncosatha.

4. Anene tsono iwo akuopa Yehova,Kuti cifundo cace ncosatha.

5. M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.

6. Yehova ndi wanga; sindidzaopa;Adzandicitanji munthu?

7. Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;M'mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,

8. Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira munthu.

9. Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira akulu,

10. Amitundu onse adandizinga,Zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

11. Adandizinga, inde, adandizinga:Indedi, m'dzinala Yehova ndidzawaduladula.

12. Adandizinga ngati njuci;Anazima ngati moto waminga;Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

13. Kundikankha anandikankha ndikadagwa;Koma Yehova anandithandiza.

14. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;Ndipo anakhala cipulumutso canga.

15. M'mahema a olungama muli liu lakupfuula mokondwera ndi la cipulumutso:

16. Dzanja lamanja la Yehova licita mwamphamvu.

17. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,Ndipo ndidzafotokozera nchito za Yehova.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 118