Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 118:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,Ndipo ndidzafotokozera nchito za Yehova.

18. Kulanga anandilangadi Yehova:Koma sanandipereka kuimfa ai.

19. Nditsegulireni zipata za cilungamo;Ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.

20. Cipata ca Yehova ndi ici;Olungama adzalowamo.

21. Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,Ndipo munakhala cipulumutso canga,

22. Mwala umene omangawo anaukanaWakhala mutu wa pangondya.

23. Ici cidzera kwa Yehova;Ncodabwiza ici pamaso pathu.

24. Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;Tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.

25. Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;Tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.

26. Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;Takudalitsani kocokera m'nyumba ya Yehova.

27. Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;Mangani nsembe ndi zingwe, ku nyanga za guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 118