Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 118:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.

2. Anene tsono Israyeli,Kuti cifundo cace ncosatha.

3. Anene tsono nyumba ya Aroni,Kuti cifundo cace ncosatha.

4. Anene tsono iwo akuopa Yehova,Kuti cifundo cace ncosatha.

5. M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.

6. Yehova ndi wanga; sindidzaopa;Adzandicitanji munthu?

7. Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;M'mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,

8. Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira munthu.

9. Kuthawira kwa Yehova nkokomaKoposa kukhulupirira akulu,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 118