Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 109:3-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo anandizinga ndi mau a udani,Nalimbana nane kopanda cifukwa.

4. M'malo mwa cikondi canga andibwezera udani;Koma ine, kupemphera ndiko.

5. Ndipo anandisenza coipa m'malo mwa cokoma,Ndi udani m'malo mwa cikondi canga.

6. Muike munthu woipa akhale mkuru wace;Ndi mdani aime pa dzanja lamanja lace.

7. Ponenedwa mlandu wace aturuke wotsutsika;Ndi pemphero lace likhale ngati kucimwa.

8. Masiku ace akhale owerengeka;Wina alandire udindo wace.

9. Ana ace akhale amasiye, Ndi mkazi wace wamasiye.

10. Ana ace akhale amcirakuyenda ndi opemphapempha;Afunefune zosowa zao kucokera m'mabwinja mwao.

11. Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;Ndi alendo alande za nchito yace.

12. Pasakhale munthu wakumdtira cifundo;Kapena kucitira cokoma ana ace amasiye.

13. Zidzukulu zace zidulidwe;Dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.

14. Mphulupulu za makolo ace zikumbukike ndi Yehova;Ndi cimo la mai wace lisafafanizidwe.

15. Zikhale pamaso pa Yehova cikhalire,Kuti adule cikumbukilo cao kucicotsera ku dziko lapansi.

16. Cifukwa kuti sanakumbukila kucita cifundo,Koma analondola wozunzika ndi waumphawi,Ndi wosweka mtima, kuti awaphe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 109