Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 109:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini;Sanakondwera nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.

18. Anabvalanso temberero ngati maraya,Ndipo lidamlowa m'kati mwace ngati madzi,Ndi ngati mafuta m'mafupa ace.

19. Limkhalire ngati cobvala adzikuta naco,Ndi lamba limene adzimangirira nalo m'cuuno cimangirire,

20. Ici cikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova,Ndi ya iwo akunenera coipa moyo wanga.

21. Koma Inu, Yehova Ambuye, mucite nane cifukwa ca dzina lanu;Ndilanditseni popeza cifundo canu ndi cabwino.

22. Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi,Ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga.

23. Ndamuka ngati mthunzi womka m'taliNdiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.

24. Mabondo anga agwedezeka cifukwa ca kusala;Ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.

25. Ndiwakhaliranso cotonza;Pakundiona apukusa mutu.

26. Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga:Ndipulumutseni monga mwa cifundo canu;

27. Kuti adziwe kuti ici ndi dzanja lanu;Kuti Inu Yehova munacicita.

28. Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu;Pakuuka iwowa adzacita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 109