Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 109:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu wa cilemekezo canga, musakhale cete;

2. Pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa cinyengo pananditsegukira;Anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.

3. Ndipo anandizinga ndi mau a udani,Nalimbana nane kopanda cifukwa.

4. M'malo mwa cikondi canga andibwezera udani;Koma ine, kupemphera ndiko.

5. Ndipo anandisenza coipa m'malo mwa cokoma,Ndi udani m'malo mwa cikondi canga.

6. Muike munthu woipa akhale mkuru wace;Ndi mdani aime pa dzanja lamanja lace.

7. Ponenedwa mlandu wace aturuke wotsutsika;Ndi pemphero lace likhale ngati kucimwa.

8. Masiku ace akhale owerengeka;Wina alandire udindo wace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 109