3. Amene alumikiza mitanda ya zipinda zace m'madzi;Naika makongwa akhale agareta ace;Nayenda pa mapiko a mphepo;
4. Amene ayesa mphepo amithenga ace;Lawi la moto atumiki ace;
5. Anakhazika dziko lapansi pa maziko ace,Silidzagwedezeka ku nthawi yonse.
6. Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi cobvala;Madzi anafikira pamwamba pa mapiri,
7. Pa kudzudzula kwanu anathawa;Anathawa msanga liu la bingu lanu;
8. Anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa,Kufikira malo mudawakonzeratu.
9. Munaika malire kuti asapitirireko;Kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.
10. Atumiza akasupe alowe m'makwawa;Ayenda pakati pa mapiri:
11. Zimamwamo nyama zonse za kuthengo;Mbidzi zipherako ludzu lao.
12. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo,Zimayimba pakati pa mitawi.
13. Iye amwetsa mapiri mocokera m'zipinda zace:Dziko lakhuta zipatso za nchito zanu.