1. Lemekeza Yehova, moyo wanga;Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkurukuru;
2. Mubvala ulemu ndi cifumu.Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi cobvala;Ndi kuyala thambo ngati nsaru yocinga;
3. Amene alumikiza mitanda ya zipinda zace m'madzi;Naika makongwa akhale agareta ace;Nayenda pa mapiko a mphepo;
4. Amene ayesa mphepo amithenga ace;Lawi la moto atumiki ace;
5. Anakhazika dziko lapansi pa maziko ace,Silidzagwedezeka ku nthawi yonse.
6. Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi cobvala;Madzi anafikira pamwamba pa mapiri,
7. Pa kudzudzula kwanu anathawa;Anathawa msanga liu la bingu lanu;