Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 103:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo.

7. Analangiza Mose njira zace,Ndi ana a Israyeli macitidwe ace.

8. Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo,Wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka.

9. Sadzatsutsana nao nthawi zanse;Ndipo sadzasunga mkwiyo wace kosatha.

10. Sanaticitira monga mwa zolakwa zathu,Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

11. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi,Motero cifundo cace cikulira iwo akumuopa Iye.

12. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo,Momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.

13. Monga atate acitira ana ace cifundo,Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.

14. Popeza adziwa mapangidwe athu;Akumbukila kuti ife ndife pfumbi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 103