Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 103:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Lemekeza Yehova, moyo wanga;Ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lace loyera.

2. Lemekeza Yehova, moyo wanga,Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:

3. Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;Naciritsa nthenda zako zonse;

4. Amene aombola moyo wako ungaonongeke;Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:

5. Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.

6. Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo.

7. Analangiza Mose njira zace,Ndi ana a Israyeli macitidwe ace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 103