Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 100:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.

2. Tumikirani Yehova ndi cikondwerero:Idzani pamaso pace ndi kumyimbira mokondwera,

3. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace;Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace.

4. Lowani ku zipata zace ndi ciyamiko,Ndi ku mabwalo ace ndi cilemekezo:Myamikeni; lilemekezeni dzina lace.

5. Pakuti Yehova ndiye wabwino; cifundo cace cimamka muyaya;Ndi cikhulupiriko cace ku mibadwo mibadwo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 100