Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 1:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,Kapena wosaimirira m'njira ya ocimwa,Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2. Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace;Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.

3. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace,Tsamba lace lomwe losafota;Ndipo zonse azicita apindula nazo.

4. Oipa satero ai;Koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5. Cifukwa cace oipa sadzaimirira pa mlanduwo,Kapena ocimwa mu msonkhano wa olungama.

6. Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;Koma mayendedwe a oipa adzatayika.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 1