Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 5:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Akapolo atilamulira;Palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.

9. Timalowa m'zoopsya potenga zakudya zathu,Cifukwa ca lupanga la m'cipululu,

10. Khungu lathu lapserera ngati pamotoCifukwa ca kuwawa kwa njala.

11. Anaipitsa akazi m'Ziyoni,Ndi anamwali m'midzi ya Yuda.

12. Anawapacika akalonga manja ao;Sanalemekeza nkhope za akulu.

13. Anyamata ananyamula mphero,Ana nakhumudwa posenza nkhuni.

14. Akulu adatha kuzipata,Anyamata naleka nyimbo zao.

15. Cimwemwe ca mtima wathu calekeka,Masewera athu asanduka maliro.

16. Korona wagwa pamutu pathu;Kalanga ife! pakuti tinacimwa.

17. Cifukwa ca ici mtima wathu ufoka,Cifukwa ca izi maso athu acita cimbuuzi;

18. Pa phiri la Ziyoni lopasukaloAnkhandwe ayendapo.

Werengani mutu wathunthu Maliro 5