Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Adandaulira Yehova pa tsoka la ukapolo wao

1. Yehova, kumbukirani cotigweraci,Penyani nimuone citonzo cathu.

2. Colowa cathu casanduka ca alendo,Ndi nyumba zathu za acilendo.

3. Ndife amasiye opanda atate,Amai athu akunga akazi amasiye.

4. Tinamwa madzi athu ndi ndalama,Tiona nkhuni zathu pozigula.

5. Otilondola atigwira pakhosi pathu,Tatopa osaona popumira.

6. Tinagwira mwendo AiguptoNdi Asuri kuti tikhute zakudya.

7. Atate athu anacimwa, kulibe iwo;Ndipo tanyamula mphulupulu zao.

8. Akapolo atilamulira;Palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.

9. Timalowa m'zoopsya potenga zakudya zathu,Cifukwa ca lupanga la m'cipululu,

10. Khungu lathu lapserera ngati pamotoCifukwa ca kuwawa kwa njala.

11. Anaipitsa akazi m'Ziyoni,Ndi anamwali m'midzi ya Yuda.

12. Anawapacika akalonga manja ao;Sanalemekeza nkhope za akulu.

13. Anyamata ananyamula mphero,Ana nakhumudwa posenza nkhuni.

14. Akulu adatha kuzipata,Anyamata naleka nyimbo zao.

15. Cimwemwe ca mtima wathu calekeka,Masewera athu asanduka maliro.

16. Korona wagwa pamutu pathu;Kalanga ife! pakuti tinacimwa.

17. Cifukwa ca ici mtima wathu ufoka,Cifukwa ca izi maso athu acita cimbuuzi;

18. Pa phiri la Ziyoni lopasukaloAnkhandwe ayendapo.

19. Inu, Yehova, mukhala cikhalire,Ndi mpando wanu wacifumu ku mibadwo mibadwo.

20. Bwanji mutiiwala ciiwalire,Ndi kutisiya masiku ambirimbiri;

21. Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi,Mukonzenso masiku athu ngati kale lija.

22. Koma mwatikaniza konse,Mwatikwiyira kopambana.