Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 5:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, kumbukirani cotigweraci,Penyani nimuone citonzo cathu.

2. Colowa cathu casanduka ca alendo,Ndi nyumba zathu za acilendo.

3. Ndife amasiye opanda atate,Amai athu akunga akazi amasiye.

4. Tinamwa madzi athu ndi ndalama,Tiona nkhuni zathu pozigula.

5. Otilondola atigwira pakhosi pathu,Tatopa osaona popumira.

6. Tinagwira mwendo AiguptoNdi Asuri kuti tikhute zakudya.

7. Atate athu anacimwa, kulibe iwo;Ndipo tanyamula mphulupulu zao.

8. Akapolo atilamulira;Palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.

9. Timalowa m'zoopsya potenga zakudya zathu,Cifukwa ca lupanga la m'cipululu,

10. Khungu lathu lapserera ngati pamotoCifukwa ca kuwawa kwa njala.

11. Anaipitsa akazi m'Ziyoni,Ndi anamwali m'midzi ya Yuda.

12. Anawapacika akalonga manja ao;Sanalemekeza nkhope za akulu.

Werengani mutu wathunthu Maliro 5