Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 4:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Omveka ace anakonzeka koposa cipale cofewa, nayera koposa mkaka,Matupi ao anafiira koposa timiyala toti pyu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatari.

8. Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala;Khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.

9. Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala;Pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.

10. Manja a akazi acisoni anaphika anaanao;Anali cakudya cao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

11. Yehova wakwaniritsa kuzaza kwace, watsanulira ukali wace;Anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ace,

12. Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirira, ngakhale onse okhala kunja kuno,Kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.

13. Ndico cifukwa ca macimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembeace,Amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pace.

14. Asocera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi;Anthu sangakhudze zobvala zao.

15. Amapfuula kwa iwo, Cokani, osakonzeka inu, cokani, cokani, musakhudze kanthu.Pothawa iwo ndi kusocera, anthu anati mwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.

16. Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;Iwo sanalemekeza ansembe, sanakomera mtima akulu.

17. Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo cabe;Kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.

18. Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;Citsiriziro cathu cayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti citsiriziro cathu cafikadi.

Werengani mutu wathunthu Maliro 4