Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 4:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Yehova wakwaniritsa kuzaza kwace, watsanulira ukali wace;Anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ace,

12. Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirira, ngakhale onse okhala kunja kuno,Kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.

13. Ndico cifukwa ca macimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembeace,Amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pace.

14. Asocera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi;Anthu sangakhudze zobvala zao.

15. Amapfuula kwa iwo, Cokani, osakonzeka inu, cokani, cokani, musakhudze kanthu.Pothawa iwo ndi kusocera, anthu anati mwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.

16. Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;Iwo sanalemekeza ansembe, sanakomera mtima akulu.

17. Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo cabe;Kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.

18. Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;Citsiriziro cathu cayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti citsiriziro cathu cafikadi.

19. Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwilo lao,Anatithamangitsa pamapiri natilalira m'cipululu.

20. Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; Amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwace pakati pa amitundu,

21. Kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dzikola Uzi;Cikho cidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kubvulazako.

22. Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende;Koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzabvumbulutsa zocimwa zako.

Werengani mutu wathunthu Maliro 4