Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 4:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ha! golidi wagugadi; golidi woona woposa wasandulika;Miyala ya malo opatulika yakhutulidwa pa malekezero a makwalalaonse.

2. Ana a Ziyoni a mtengo wapatari, olingana ndi golidi woyengetsa,Angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

3. Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;Koma mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'cipululu.

4. Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwace ndi ludzu;Ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

5. Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;Omwe analeredwa nabvekedwa mlangali afungatira madzala.

6. Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga, ikula koposa cimo la Sodomu,Umene unapasuka m'kamphindi, anthu osaucitira kanthu.

Werengani mutu wathunthu Maliro 4