Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 2:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Yehova wacita comwe analingalira;Watsiriza mau ace, amene analamulira nthawi yakale;Wagwetsa osacitira cisoni;Wakondweretsa adani pa iwe,Wakweza nyanga ya amaliwongo ako.

18. Mtima wao unapfuula kwa Ambuye,Linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;Usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.

19. Tauka, tapfuula usiku, poyamba kulonda;Tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;Takwezera maso ako kwa Iye, cifukwa ca moyo wa tiana tako,Timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.

20. Onani Yehova, nimupenye, mwacitira ayani ici?Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawaseweza?Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?

21. Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala;Anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;Munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osacitira cisoni.

22. Mwaitana zondiopsya mozungulira ngati tsiku la msonkhano;Panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;Omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.

Werengani mutu wathunthu Maliro 2