20. Onani, Yehova; pakuti ndabvutika, m'kati mwanga mugwedezeka;Mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu;Kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.
21. Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza;Adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu;Mudzafikitsa tsiku lija mwalichula, ndipo iwowo adzanga ine.
22. Zoipa zao zonse zidze pamaso panu,Muwacitire monga mwandicitira ine cifukwa ca zolakwa zanga zonse,Pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga,