Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Malaki 4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Oipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale cilamulo; adzafika Eliya

1. Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akucita coipa, adzakhala ngati ciputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.

2. Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la cilungamo lidzakuturukirani, muli kuciritsa m'mapiko mwace; ndipo mudzaturuka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng'ombe onenepa,

3. Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wamakamu.

4. Kumbukilani cilamulo ca Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliraco m'Horebu cikhale ca Israyeli lonse, ndico malemba ndi maweruzo.

5. Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikuru ndi loopsa la Yehova.

6. Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.