Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 9:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa cihema cokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova,

6. Ndipo Mose anati, Ici ndi cimene Yehova anakuuzani kuti mucicite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

7. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yaucimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzicitire wekha ndi anthuwo cotetetezera; nupereke coperekaca anthu, ndi kuwacitira cotetezera; monga Yehova anauza.

8. Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwana wa ng'ombe wa nsembe yaucimo, ndiyo ya kwa iye yekha.

9. Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anabviika cala cace m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde pa guwa la nsembe;

10. koma mafutawo, ndi imso, ndi cokuta ca mphafa za nsembe yaucimo, anazitentha pa guwa la nsembe; monga Yehova anauza Mose.

11. Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi cikopa kunja kwa cigono.

12. Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozu ngulira.

13. Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, ciwalo ciwalo, ndi mutu wace; ndipo anazitentha pa guwa la nsembe.

14. Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza pa guwa la nsembe.

15. Ndipo anabwera naco copereka ca anthu, natenga mbuzi ya nsembe yaucimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yaucimo, monga yoyamba ija.

16. Ndipo anabwera nayo nsembe yopsereza naipereka monga mwa lemba lace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 9