Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 8:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ace, nawasambitsa ndi madzi,

7. Ndipo anambveka ndi maraya a m'kati, nammanga m'cuuno ndi mpango, nambveka ndi mwinjiro, nambveka ndi efodi, nammanga m'cuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pace.

8. Ndipo anamuika capacifuwa; naika m'capacifuwa Urimu ndi Tumimu.

9. Naika nduwirayo pamutu pace; ndi panduwira, pamphumi pace anaika golidi waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10. Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza kacisi, ndi ronse ziti m'mwemo, nazipatula.

11. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace, kuzipatula.

12. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula,

13. Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawabveka maraya a m'kati, nawamanga m'cuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adauza Mose.

14. Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yaucimo.

15. Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi cala cace pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alicitire colitetezera.

16. Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 8