Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 8:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza kacisi, ndi ronse ziti m'mwemo, nazipatula.

11. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace, kuzipatula.

12. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula,

13. Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawabveka maraya a m'kati, nawamanga m'cuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adauza Mose.

14. Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yaucimo.

15. Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi cala cace pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alicitire colitetezera.

16. Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe.

17. Koma ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi nyama yace, ndi cipwidza cace, anazitentha ndi mote kunja kwa cigono; monga Yehova adamuuza Mose.

18. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19. Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

20. Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zace; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21. Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 8