Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:31-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo pa guwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Arent ndi ana ace.

32. Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe, ukhale nsembe yokweza yocokera ku nsembe zoyamika zanu.

33. Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lace la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera Ilao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.

34. Pakuti ndatengako kwa ana a Israyeli, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ace, zikhale zoyenera iwo kosatha zocokera kwa ana a Israyeli.

35. Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ace, locokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;

36. limene Yehova anauza ana a Israyeli aziwapatsa, tsiku limene iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

37. Ico ndi cilamulo ca nsembe yopsereza, ca nsembe yaufa, ca nsembe yaucimo, ndi ca nsembe yoparamula, ndi ca kudzaza dzanja, ndi ca nsembe zoyamika;

38. cimene Yehova analamulira Mose m'phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israyeli abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m'cipululu ca Sinai.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7